Psalms 110

Salimo la Davide.

1Yehova akuwuza Mbuye wanga kuti,
“Khala ku dzanja langa lamanja
mpaka nditasandutsa adani ako
kukhala chopondapo mapazi ako.”

2Yehova adzakuza ndodo yamphamvu ya ufumu wako kuchokera mʼZiyoni;
udzalamulira pakati pa adani ako.
3Ankhondo ako adzakhala odzipereka
pa tsiku lako la nkhondo.
Atavala chiyero chaulemerero,
kuchokera mʼmimba ya mʼbandakucha,
udzalandira mame a unyamata wako.

4Yehova walumbira
ndipo sadzasintha maganizo ake:
“Ndiwe wansembe mpaka muyaya
monga mwa unsembe wa Melikizedeki.”

5Ambuye ali kudzanja lako lamanja;
Iye adzaponda mafumu pa tsiku la ukali wake.
6Adzaweruza anthu a mitundu ina,
adzadzaza dziko lapansi ndi mitembo ndipo adzaphwanya olamulira a pa dziko lonse lapansi.
7Iye adzamwa mu mtsinje wa mʼmbali mwa njira;
choncho adzaweramutsa mutu wake.
Copyright information for NyaCCL